Categories
Sin categoría

Mawa


Tradutor: Kondwani Bewala
Língua: Cinyanja, Moçambique

Tikukumbukira za izi ngati zinachitika dzulo
ndikanazicha dzina la “Phunzitso Lalikulu” m’mabuku a nkhani zakale
Ndipo panali pamenepo pamene zinthu zonse zinayamba kusintha,
Dziko limene tinali kulidziwa m’pakani pano, zimene timaziwona kukhala zololedwa, “La
normalité”, kacitidwe ka zinthu kamene kamayika anthu onse pangozi ya kufa.

M’masiku ocepa anthu zikwi-zikwi adayamba kufa padziko lonse lapansi, m’midzi
yolemera ndi yosawuka.
Ambili anali anthu omwe akadayenera kukhala amoyo lero, tikadakhala okonzekera…
Tidazindikira kuti izi sizinali zacilendo, pomwe tidawona kuti timasowa mabedi kotero
anthu adamwalira, pomwe timayamba kusowa zida zopumira, tinazindikira kuti tinalibe
citetezo cokwanira, patapita nthawi.
Tonse timakhala n’nyumba zathu kuti kuti tipewe kuluza moyo
Ndipamene ndinayama kulemba mavesi ngati odzipereka, kwa anthu okhudzidwa.

Panthawiyi, imfa idapitilirabe kufalikira padziko lapansi malamulo, mipanda, waya
wochigidwa komanso nyanja, magulu a nkhondo ndi apolisi zonse zinali za pacabe
Kwa nthawi yoyamba timadziwa za cina cake comwe cingacedwetse kayendetsedwe kake
komwe kali mbali yayikulu kwa ife
Tinkawona modabwitsa pawayilesi ya kanema anthu a mayiko a mphamvu ali m’mizele
kufuna cakudya, ena m’misewu, ena ali m’makampeni a zipatala…

Dondonsolo la zinthu silinapangidwe kuti litipulumutse, silinaticenjeza panthawi yokwanira,
ngakhale kuti nthawi yake yofika imayembekezeredwa.
Dondosolo la dziko linangodikilira kacilombo mosakonzekera, mwawukapolo,
mosadzikhululukira.
Koma kucokera ku m’mawa kupita kumadzulo, kum’ponto kupita ku m’mwera dongosolo la
zinthu limene anthu adakoza silinkathandiza, ndipo pamenopo anthu sanali kugwiritsa
nchito zinthu zawo “anali kufa m’misewu ndi n’zinyumba za azigogo awo”, anatero iwo
Osawuka anali kufa mofulumira ndi mwacangu, koma ngakhale Cuma ca nkhani-nkhani
cinalipo sicimathandiza kuti munthu akhale ndi moyo.
Tinazindikira kuti, mwina kwa nthawi yoyamba, yankho si m’mene monga anatiphunzitsira,
kudzipulumutsa, koma kuti njira yopulumutsira ife inali kupulumutsa onse.

Cifukwa cake comwe tikanacicha “ciwopsezo cacikulu” cinapezeka pakati pathu, momveka
kuposa kale.
Kuti ocepa okha ndi omwe ali ndi Cuma cambiri monga dziko lonse lapansi lidayamba
kukhala n’sampha kwa onse.
Anthu ambiri padziko analibe zida zokwanira zolimbanirana ndi kacilombo kamene kanali
kuwononga ca n’kati-kati ndipo kunali kutekeseka kwa padziko lonse limene tinali kukhala
komwe kudatiweruza. Sitikanakwanitsa kukayimitsa, ngakhale ife, kudziko lapansi
lomangidwa ndi wamphamvu yonse munthu waciyera wa ku m’pototinalibe ndalama.

Cifukwa ciyani timayika kupanga zinthu, kudzipindulitsa, kugwiritsa nchito…pamaso pa
anthu, cilengedwe, moyo, wa m’mudzi kwa zaka makumi ambiri?
Ndi cifukwa ciyani tidamanga, mwa kukonza malamulo, miyambo ndi tsinde lake,
dongosolo lonseli pazolinga zakuzunza ndi kugwilira amayi?

Coyipa kwakukulu, tinakwanisa bwanji kukhala ndi izi kwa nthawi yayitali?
Bwanji tinayika “zina” tisanayike “onse”? Kodi timadya bwanji zakudya zomwe
tikanakwanisa kupanga konkuno, zomwe zimabwera ndi ndege ndi zombo ku mayiko onse
a pansi?
Ndi Cuma coculuka m’manja mwa ocepa, tonse sitinali ndi zofunika kuti tikhale ndi moyo?
Ndikukumbukira pomwe masabata angapo zisanacitike izi, pafupi ndi nyumba yanga,
ogwira nchito awiri adayikiridwa m’manda a pansi pa zinyalala za bafa. Ili linali ngati
cenjezo, fanizo la khalidwe limene linalipo nthawi imeneyo.
Cili conse, cololedwa komanso cokhazikika m’moyo wathu, cinatembenukira kwa ife pakati
pa m’liri.
Kodi anali kutani ndi ife?

Titatsekedwa kunyumba, tinazindikira kuti zinthu zonse zakalezi sizitithandizanso.
Malonda ambiri a pa TV samapezekanso.
M’masabata amenewo, sitinalinso ogula amene tinali kale. Zovomerezeka zathu komanso
tsinde lathu la cisangalo ndi mphamvu zinali zitagwa, cinthu cofunikira sicinali zomwe
zakakhala zikugulitsidwa kwa ife nthawi zonse…..osati zonse zomwe zimayenera
kupulumutsa miyoyo.
Zabwino komanso zoyipa kwambiri zathu zidatuluka, oculukidwa, osowa, maluso obisika,
maloto ndi mizukwa.
Tinagwilitsitsa nyimbo, mabuku, mafilimu, makanema kuti tisagwe…..anthu ambiri amadzia
malire awo. ena adawaswa.
Zimawoneka ngati filimu yopeka mwa sayansi, koma osati nthano cabe.
Ndinapitiliza kulandira mapempo a mavesi kwa anzanga ndi acibale amene adakhudzidwa
ndi izi: Odwala otalikilana, ogwira nchito ya zawumoyo, akufa, amayi oyembekezera, ana
acisoni, mavuto a mitundu yonse, mibadwo. Ndinazindikira kuti TV siyikuwonetsa kukula
kwa seweroli. Nthawi zina ndimalira ndili kulemba mavesiwa.
Ndipo pokhala ndi kunyalanyaza miyoyo yathu, tinayamba kucitapo kanthu, kuti tiyambe
kudzisamalira komanso kumvetsetsa moyo n’dera lathu.
Tinayamba kupanga zinda zathu zopulumutsira moyo m’mafakitale ndi m’masitolo
ang’ono-ang’ono, tinakhazikitsa njira zatsopano za m’maganizo, za uzika, ndi za citetezo
kwa wina ndi n’zake monga kale…kunali kuphuka kwa moyo watsopano. Lero, zonsezi ndi
gawo la colowa comwe tatsala naco pa “Phunzitro lalikulu”.

Komabe, akufa ndi odwala anapitilizabe kudziphatika ku zikwi.
Ku New York, anasokoneza manda
Ku n’zinda wa Guayaquil anthu anali kugwa m’misewu.
Ku Lombardy, magalimoti ankhondo odzadza ndi mabokosi amadutsa um n, zinda
Ku Madrid anthu akufa anawawunjika mu m’magalawundi ndi n’nyumba zacifumu fizi.

Ndipo zinali kuwululika powona m’mene timafera ndipo minofu yathu yonse inali kugwa,
cilengedwe cimawukitsidwa…
Mitsinje inali kuyeretsedwa
Dziko linali kuvunda
M’pweya unali kutsukidwa
Kumwamba kunali kutsukidwa
Nyanja zinali kupuma padziko lonse lapansi
M’malo ovuta aja, odayamba kuyenda bwino.

Koma timangofuna zinthu zofunikira basi: kupuma, kukumbatirana, kupitiriza kusamalira
nyumba, kuceza ndi anthu, ndi kugula zakudya.

Koma kacitidwe ka zinthu sikanayime, zinali zinthu zongodziwa kudya basi ndipo
zizimadziwa kuti zingayimitse bwani cinthu cili conse. Zinatimeza, kuyambira anthu
osawuka m’pakani kufika kwa anthu aja amadzitenga kukhala opata.

Kusiyapo ku nyumba, pamene dzuwa linaluma, kunali kuyimba, kuwomba m’manja,
kunyadira, uthenga ndi maliro zinali zosowa.
Ndinamva nkhani zakuti anthu ena odwala, amene ndawalembela mavesi, anali
kumwalira.

Ndipo zocitika pambuyo pa nthenda zinali zoyipa kuposera nthenda imene.

Mosayembekezeka, zonse zimene tinkaziwona ngati zolemera zinatitenga, kutimiza
cifukwa sitikanakwanisa kuzithandiza. Ndipo kacitidwe ka zinthu kake kanali
kusakhululuka.

Omwe amayendetsa makinawo anacitanso kanthu, pofuna kumaliza kutseka mwacangu
mabowo omwe n’dziko lapansi, anthu asanakwiye kwenikweni. Pakuti, mwina panalibe
amene adayamba waziwona izi, dongosolo lalikulu ndi mphamvu zake zinali
kugwedezeka.

Ambiri amakumbukira kuti anali atachenjezedwa,
Ena ambiri analuza zonse…
Cowonadi ndi cakuti, atakumani ndi izi, kunapangidwa gulu latsopano losakanikana ndi
anthu, anthu okwiya, omenyedwa, athu odziwa zikhalidwe ndi malingaliro zosiyana-siyana.
Maganizo akulu a padziko lonse lapansi omwe amati: ayi. Zatha.
Kuti sizingapitilire motere.

Vuto la padziko lapansi lidasinthiratu zonse. Losayiwalika. Zocitika pambuyo ndi pa
tsogolo pake zonse zidasintha.
Tinanena kuti zinali zokwanira kutha phumi tinakuwona, kumaliza ka ziwonetsero ndi
cidziwitso ca banki m’manja ndi nyimbo,
ndi kalata ya kucotsedwa, ndi kalata ya kuthamangitsidwa pamaso pa mawulamuliro
pamaso pa mabungwe akulu-akulu
pamaso pa mabokosi ocotsa abale athu
Iwo omwe alibe ciliconse coti ataye, iwo omwe anataya cili conse komanso amene
sanafune kutaya
padziko lonse lapansi cili conse cinagwedezeka
sizinacitikenso.

Anthu oculukiraculukirapo adazindikira kuti njira yothetsera movuto sinali kungotseka
mavuto basi ndi kuti tibwelere ku dongosolo lakale, koma kunali kupeza zosowa za kale
kuti tithane nazo.
Dziko linatipempha kuti tiyime kalekale koma sitinatero ndipo pano tayima, tikulipira ndi
miyoyo yathu.
Tidayamba kumvetsetsa kuti zonse dni cimodzi ndipo cimodzi ndi zonse, kuti moyo wathu
unali kupha palaneti ino, ndipo, motero kagwilitsidwe nchito kathu kopanda malire ndi
citukuko cathu cosathandiza.

Ona kuti moyo wa ife tonse padziko ndi ofunika mofanana ndipo cita mofanamo.
Kuti kupita patsogolo kwa tsinde la cimwemwe ndi kukhala kwa pawubwino, kwa
cilungamo pa anthu, kuti zinthu zonse zisinthe…

Zinali ngati ndikuwonetsetsa, tsiku loyamba la masika kunazizira.
Zinali zosangalatsa kuwona kubadwa kwa zomwe tsopano timazicha “Zatsopano za anthu
ambiri” kayendedwe ka moyo watsopano, kamene kadayika moyo patsogolo, pamene ena
um n’diz la citetezo amafuna kumadula ufulu wa patsinde wa anthu ndi kupanaga gulu
locepa la anthu komanso losungidwa.
Nkhondo yamuyaya, yomwe siyitha ndipo sidzatha.
Ayi dziko silinali ndi pulani ina ndipo palibe aliyende wa ife angakhale ndi moyo kawiri.
Anthu oculukirapo amalankhula mokwanira ndipo “Kusintha kwa moyo”kunayambika.

Tinapempha udindo, maboma akanayamba kugwa pakapita nthawi apa ndi apo…
Tinayamba kusintha moyo wathu.
Sizinali zophweka, koma mantha, zowawa, cikondi, zokumana nazo pamoyo, n’kwiyo,
zosowa, maloto, ndi cikumbuntima zonse pamodzi ndi mphanvu yosagonjetsedwa n’kati
mwathu mwa aliyense imene imatigwilizanitsa ndi kupititsa patsogolo dziko.

Tsopano zinthu zasintha. Ndife opanda angwiro, ndi nchito yomwe siyima, iyi ya moyo.
Koma ngakhale zaka zambiri zapita, sitinayiwale “phunziro lalikulu”. Tsopano, ana athu
akazi abadwira pakagawo kadziko kakang’ono kamene tsiku lina tinakwanisa kutika moyo
pamalo ake. Panopa, awo ali pamalo ake.
Katemera wolimbana ndi matendawa adafika, koma tidasankha, kamodzi ndi kamodzi kuti
tigwire tsinde lake.
Phunzilo lalikululi limaphunzitsidwa m’masukulu, kuti izi zisacitikenso.
Zaka zapita.
Nthawi imeneyozidawoneka ngati zosatheka, koma tidawona mwayi, tidakhulupilira,
tidamenyera nkhondo ndipo tsopano ndi cowonadi cathu.

Lero, tsiku loyamba la cilimwe, ndakumbukira za zonse izi ndipo ndayamba kulemba.
Zikuwoneka kuti tsiku lokongola la Epulayelo likufika. Ndikumva ana akusewera pansewu.

Ife tikukwanisa kusintha dziko
Zikuwoneka ngati maloto, koma ayi, simaloto.
Komanso lero n’tsinje ndi oyela ndipo mavesi onse amene ndinawawumba masiku aja kwa
anthu ambiri ndidakali nawo mu n’tima mwanga.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *